Ndipo anthu anatsutsana ndi Mose, nanena, nati, Mwenzi titangomwalira muja abale athu anamwalira pamaso pa Yehova!
Numeri 14:36 - Buku Lopatulika Ndipo amunawo, amene Mose anawatumiza kukazonda dziko, amene anabwera nadandaulitsa khamu lonse pa iye, poipsa mbiri ya dziko, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo amunawo, amene Mose anawatumiza kukazonda dziko, amene anabwera nadandaulitsa khamu lonse pa iye, poipsa mbiri ya dziko, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu amene Mose adaŵatuma kuti akazonde dziko aja atabwerako, ena adayamba kuutsa mitima ya anthu kuti aukire Mose pakuŵauza zoipa za dzikolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anthu amene Mose anawatuma kukazonda dziko aja anachoka pamaso pake nachititsa gulu lonse la anthu kuwukira Moseyo chifukwa chofalitsa mbiri yoyipa ya dzikolo. |
Ndipo anthu anatsutsana ndi Mose, nanena, nati, Mwenzi titangomwalira muja abale athu anamwalira pamaso pa Yehova!