Numeri 14:29 - Buku Lopatulika mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwani konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu muno. Anthu onse, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, amene adandiŵiringulira, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mitembo yanu idzakhala ili ngundangunda mʼchipululu muno; mtembo wa munthu aliyense pakati panu amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, amene anawerengedwa pa chiwerengero chija ndipo anangʼungʼudza motsutsana nane. |
ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawatulutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israele; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Potero owerengedwa onse a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo mu Israele;
inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.
Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'chipululu cha Sinai.
Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira.
Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.
Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.