Numeri 14:28 - Buku Lopatulika Nunene nao, Pali Ine ati Yehova, ndidzachitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nunene nao, Pali Ine ati Yehova, ndidzachitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uŵauze kuti, Chauta akunena kuti, ‘Zimene mwanena, Ine ndamva, ndipo ndi zimene ndidzakuchitani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono awuze kuti, ‘Ndikulumbira pali Ine,’ akutero Yehova, ‘Ndidzakuchitirani zinthu zonse zimene ndamva inu mukunena: |
Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzachitika, osazengerezekanso; pakuti m'masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwachita, ati Yehova Mulungu.
Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.
Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!
sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo ao, ngakhale mmodzi wa iwo akundinyoza Ine, sadzaliona;
Anthu adakwerawo kutuluka mu Ejipito, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; popeza sananditsate Ine ndi mtima wonse;
Palibe mmodzi wa anthu awa a mbadwo uno woipa adzaona dziko lokomalo ndinalumbira kupatsa makolo anuli.
Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira.
Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?