Potero Iye adati awaononge, pakadapanda Mose wosankhika wake, kuima pamaso pake pogamukapo, kubweza ukali wake ungawaononge.
Numeri 14:20 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati, Ndakhululukira monga mwa mau ako: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati, Ndakhululukira monga mwa mau ako: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adati, “Ndaŵakhululukira chifukwa cha mau ako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anayankha kuti, “Ndawakhululukira monga wapemphera. |
Potero Iye adati awaononge, pakadapanda Mose wosankhika wake, kuima pamaso pake pogamukapo, kubweza ukali wake ungawaononge.
Munawayankha, Yehova Mulungu wathu: munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira, mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao.
Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'mtsinje mokha?
Atero Yehova, Anthu opulumuka m'lupanga anapeza chisomo m'chipululu; Israele, muja anakapuma.
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.