Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.
Numeri 14:17 - Buku Lopatulika Ndipo tsopano, ikuletu mphamvu ya Mbuye wanga, monga mudanena, ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsopano, ikuletu mphamvu ya Mbuye wanga, monga mudanena, ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ndikukupemphani, Chauta muwonetse kuti mphamvu zanu nzazikulu monga mudalonjezera kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Chonde Ambuye wonetsani mphamvu yanu monga munalonjezera kuti, |
Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.
Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa anthu awa m'dziko limene anawalumbirira, chifukwa chake anawapha m'chipululu.
Yehova ndiye wolekereza, ndi wa chifundo chochuluka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula wopalamula; wakuwalanga ana chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa Munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge mphasa yako, numuke kunyumba kwako.
Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.