Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa ndi cholinga choipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope padziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu.
Numeri 14:15 - Buku Lopatulika Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepo amitundu amene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepo amitundu amene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsopano mukaŵapha onse anthu ameneŵa, mitundu ina imene yamva mbiri yanu idzati, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono mukawapha anthu onsewa nthawi imodzi, mayiko amene anamva za Inu adzati, |
Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa ndi cholinga choipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope padziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu.
Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa anthu awa m'dziko limene anawalumbirira, chifukwa chake anawapha m'chipululu.
Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidiyani ngati munthu mmodzi.