Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 11:33 - Buku Lopatulika

Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyama ikadali m'kamwa mwao, asanaimeze nkomwe, Chauta adaŵapsera mtima anthuwo, ndipo adaŵagwetsera mliri woopsa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma pamene anthuwo ankadya nyamayo, asanayimeze nʼkomwe, ukali wa Yehova unafika pa iwo ndipo Iye anawakantha ndi mliri woopsa.

Onani mutuwo



Numeri 11:33
10 Mawu Ofanana  

chinkana achisunga, osachileka, nachikhalitsa m'kamwa mwake;


Poti adzaze mimba yake, Mulungu adzamponyera mkwiyo wake waukali, nadzamvumbitsira uwu pakudya iye.


Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa, natsogoza mwera ndi mphamvu yake.


Potero anadya nakhuta kwambiri; ndipo anawapatsa chokhumba iwo.


Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera chija cha Kora.


Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza, momwemo anachita.


Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai.


Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo.