Numeri 11:31 - Buku Lopatulika Ndipo kudachokera mphepo kwa Yehova, n'kudza nazo zinziri zochokera kunyanja, ndipo zidagwa kuchigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa chigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kudachokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zochokera kunyanja, nizitula kuchigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa chigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adautsa mphepo kuchokera ku nyanja. Mphepoyo idabwera ndi zinziri, ndipo zidagwera pafupi ndi mahema. Kuchokera kumahemako, zinzirizo zidagwa pa mtunda woyenda ulendo wa tsiku limodzi mbali imodzi, mbali inanso chimodzimodzi, mozungulira mahemawo. Zitaunjikana, mjintchi wake unali ngati mita limodzi kuchokera pansi mpaka pamwamba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Yehova anawutsa mphepo yochokera ku nyanja imene inabweretsa zinziri. Zinzirizo zinagwera pansi kuzungulira msasa, mtunda wa kilomita imodzi mbali zonse ndipo msinkhu wake unali mita imodzi. |
Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi; ang'animitsa mphezi zidzetse mvula; atulutsa mphepo mosungira mwake.
Pamenepo Mose analoza ndodo yake padziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe.
Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.
Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m'mawa padagwa mame pozungulira tsasa.