Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 11:27 - Buku Lopatulika

Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m'chigono.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m'chigono.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndiye mnyamata wina adathamanga nakauza Mose kuti, “Elidadi ndi Meladi akulosa kumahemaku.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mnyamata wina anathamanga kudzawuza Mose kuti, “Elidadi ndi Medadi akunenera mu msasa.”

Onani mutuwo



Numeri 11:27
4 Mawu Ofanana  

Koma amuna awiri anatsalira m'chigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzake ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanatuluke kunka kuchihema; ndipo ananenera m'chigono.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.


Yohane anati kwa Iye, Mphunzitsi, tinaona munthu alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa sanalikutsata ife.


Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa satsatana nafe.