Nati, Ndaniyo atuluka ngati mbandakucha, wokongola ngati mwezi, woyera ngati dzuwa, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera?
Numeri 10:28 - Buku Lopatulika Potero maulendo a ana a Israele anakhala monga mwa magulu ao; nayenda ulendo wao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potero maulendo a ana a Israele anakhala monga mwa magulu ao; nayenda ulendo wao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Umenewu ndiwo mndandanda wa kayendedwe ka Aisraele, pamene ankanyamuka ulendo wao m'magulumagulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Umenewu ndiwo unali mndandanda wa kayendedwe ka magulu a Aisraeli pamene ankanyamuka ulendo wawo mʼmagulumagulu. |
Nati, Ndaniyo atuluka ngati mbandakucha, wokongola ngati mwezi, woyera ngati dzuwa, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera?
Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma.
Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake.
pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.
Pakuti ndingakhale ndili kwina m'thupi, komatu mumzimu ndili pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Khristu.