Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israele, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lake.
Numeri 1:45 - Buku Lopatulika Potero owerengedwa onse a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo mu Israele; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potero owerengedwa onse a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo m'Israele; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho amuna onse a mu Israele otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata banja la makolo ao, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli anawawerenga monga mwa mabanja awo. |
Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israele, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lake.
inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.
mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwani konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;