Nehemiya 9:6 - Buku Lopatulika Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Ezara adapemphera kuti, “Inu nokha ndiye Chauta. Inu mudalenga kumwamba, kumwambamwamba, ndiponso zonse zokhala komweko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Mudalenga nyanja ndi zonse zam'menemo. Zonse zakumwamba zimakupembedzani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani. |
Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pakumwamba asonkhane pamodzi pamalo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero.
Pamene Yakobo anawaona anati, Ili ndi khamu la Mulungu: ndipo anatcha pamenepo dzina lake Mahanaimu.
Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.
Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.
Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israele wakukhala pakati pa akerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wake, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokhanokha.
Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.
Amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha,
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Chifukwa chake, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m'manja mwake, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.
Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina.
Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.
Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa lililonse.
Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za m'menemo, ndinazilamulira ndine.
Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;
Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo.
Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.
Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili m'menemo;
Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo ndi zake za Yehova Mulungu wanu.
Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.
ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,
Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu.
ndi kunena ndi mau aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe amadzi.
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.