Nehemiya 9:21 - Buku Lopatulika Ndipo munawalera zaka makumi anai m'chipululu, osasowa kanthu iwo; zovala zao sizinathe, ndi mapazi ao sanatupe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo munawalera zaka makumi anai m'chipululu, osasowa kanthu iwo; zovala zao sizinatha, ndi mapazi ao sanatupe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudaŵasunga zaka makumi anai m'chipululu ndipo nthaŵi yonseyo sankasoŵa kanthu. Zovala zao sizidathe, mapazi aonso sadatupe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munawasunga zaka makumi anayi mʼchipululu ndipo sanasowe kanthu kalikonse. Zovala zawo sizinathe kapena mapazi awo kutupa.” |
Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.
Ngati munabwera nazo kwa Ine nsembe zophera ndi zaufa zaka makumi anai m'chipululu, inu nyumba ya Israele?
Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowe kanthu.
Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu; zovala zanu sizinathe pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinathe pa phazi lanu.
Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.