Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.
Nehemiya 9:18 - Buku Lopatulika Ngakhale apa atadzipangira mwanawang'ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kuchokera ku Ejipito, nachita zopeputsa zazikulu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ngakhale apa atadzipangira mwanawang'ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kuchokera ku Ejipito, nachita zopeputsa zazikulu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngakhale pamene adadzipangira fano la mwanawang'ombe, namanena kuti, ‘Uyu ndiye Mulungu wathu amene adatitulutsa ku dziko la Ejipito,’ ndipo ngakhale adachita zinthu zoipitsitsa zokunyozani, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale pamene iwo anadziwumbira fano la mwana wangʼombe ndi kuti, ‘Uyu ndi mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto,’ kapena pamene anachita chipongwe choopsa. |
Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.
Ngati munabwera nazo kwa Ine nsembe zophera ndi zaufa zaka makumi anai m'chipululu, inu nyumba ya Israele?