koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.
Nehemiya 9:12 - Buku Lopatulika Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munkaŵatsogolera masana ndi mtambo, ndipo usiku munkaŵaunikira ndi moto njira imene ankayendamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Masana munkawunikira ndi chipilala cha mtambo ndipo usiku munkawunikira ndi chipilala cha moto njira yonse imene ankayendamo. |
koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.
Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola; mwamphamvu yanu mudawalondolera njira yakunka pokhala panu poyera.
tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, kunka nao kudziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;
Koma mtambo ukakhala kuyambira madzulo kufikira m'mawa; pokwera mtambo m'mawa, ayenda ulendo.
amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi moto usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.