Anasanduliza nyanja ikhale mtunda. Anaoloka mtsinje choponda pansi, apo tinakondwera mwa Iye.
Nehemiya 9:11 - Buku Lopatulika Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudagaŵa nyanja pakati, anthu anu akupenya, kotero kuti iwowo adaoloka pakati pa nyanja pali pouma. Kenaka mudaŵamiza m'nyanja adani amene ankaŵalondola, monga momwe umachitira mwala m'madzi ozama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu munagawa nyanja anthu anu akupenya, kotero kuti anadutsa powuma, koma munamiza mʼmadzi akuya anthu amene ankawalondola monga mmene uchitira mwala mʼmadzi ozama. |
Anasanduliza nyanja ikhale mtunda. Anaoloka mtsinje choponda pansi, apo tinakondwera mwa Iye.
Ndipo anagulula njinga za magaleta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aejipito anati, Tithawe pamaso pa Israele; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aejipito.
Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere.
amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, mu Israele ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;
Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;
Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aejipito poyesanso anamizidwa.
Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala ngati mphero yaikulu, naiponya m'nyanja, nanena, Chotero Babiloni, mzinda waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.