Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.
Nehemiya 8:11 - Buku Lopatulika Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli chete; pakuti lero ndi lopatulika; musamachita chisoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli chete; pakuti lero ndi lopatulika; musamachita chisoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Alevi adacheteketsa anthu onse naŵauza kuti, “Musalirenso ai, pakuti lero ndi tsiku loyera, choncho musakhale ndi chisoni.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alevi anakhalitsa bata anthu onse powawuza kuti, “Khalani chete, pakuti lero ndi tsiku lopatulika ndipo musakhale ndi chisoni.” |
Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.
Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera.
Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.