Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani, Imeri, ndi awa, koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisraele:
Nehemiya 7:61 - Buku Lopatulika Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israele; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israele; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ali m'munsiŵa ndiwo amene adabwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni ndi ku Imeri, ngakhale sankatha kutsimikiza kuti makolo ao kapena mafuko ao analidi Aisraele enieni kapena ai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi. |
Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani, Imeri, ndi awa, koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisraele:
Antchito onse a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.
ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri.