Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwaomwao m'mizinda mwao, ndiwo Israele, ansembe, Alevi, ndi Antchito a m'kachisi.
Nehemiya 7:60 - Buku Lopatulika Antchito onse a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anetini onse, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Antchito onse a ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo zidzukulu za antchito a Solomoni, onse pamodzi analipo 392. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo 392. |
Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwaomwao m'mizinda mwao, ndiwo Israele, ansembe, Alevi, ndi Antchito a m'kachisi.
Antchito onse a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.
Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israele;