Alevi: ana a Yesuwa, ndi Kadimiyele, ndiwo a ana a Hodaviya, makumi asanu ndi awiri mphambu anai.
Nehemiya 7:43 - Buku Lopatulika A Levi: ana a Yesuwa, a Kadimiyele, a ana a Hodeva, makumi asanu ndi awiri kudza anai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 A Levi: ana a Yesuwa, a Kadimiyele, a ana a Hodeva, makumi asanu ndi awiri kudza anai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Alevi anali aŵa: a banja la Yesuwa ndi la Kadimiyele, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya, 74. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alevi anali awa: A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya 74. |
Alevi: ana a Yesuwa, ndi Kadimiyele, ndiwo a ana a Hodaviya, makumi asanu ndi awiri mphambu anai.
Awa tsono ndi akulu a dziko okhala mu Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi antchito a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni.
Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko.
Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu.