Nehemiya 6:5 - Buku Lopatulika Pamenepo Sanibalati anatuma mnyamata wake kwa ine kachisanu, ndi kalata yosatseka m'dzanja mwake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Sanibalati anatuma mnyamata wake kwa ine kachisanu, ndi kalata wosatseka m'dzanja mwake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Sanibalati adatumanso wantchito wake kachisanu kwa ine. Iye anali ndi kalata yosamata m'manja mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono kachisanu, Sanibalati anatumiza wantchito wake ndi kalata yosamata. |
m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gesemu achinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; chifukwa chake mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa.
Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.
ndi m'chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza chikondi cha choonadi sanachilandire, kuti akapulumutsidwe iwo.