Chifukwa chake ndinawaika potera m'kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao.
Nehemiya 6:3 - Buku Lopatulika Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindingathe kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindikhoza kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake ndidaŵatumira amithenga kukaŵauza kuti, “Ine kuno ndili pa ntchito yaikulu, sindingathe kuchoka kuti ndibwere kumeneko. Kodi ntchito iime, pofuna kuti ndibwere kumeneko?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho ine ndinatuma amithenga ndi yankho ili: “Ine ndikugwira ntchito yayikulu kuno ndipo sindingathe kubwera kumeneko. Kodi ntchito iyime pofuna kuti ndibwere kumeneko?” |
Chifukwa chake ndinawaika potera m'kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao.
anatumiza mau kwa ine Sanibalati ndi Gesemu, kuti, Tiyeni tikomane kumidzi ya ku Chigwa cha Ono; koma analingirira za kundichitira choipa.
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.