Anamlembera chifukwa cha ichi, kuti ine ndichite mantha, ndi kuchita chotero, ndi kuchimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.
Nehemiya 6:19 - Buku Lopatulika Anatchulanso ntchito zake zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza makalata kuti andiopse ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anatchulanso ntchito zake zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza akalata kuti andiopse ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ankasimba za ntchito zabwino za Tobiyayo ine ndili pomwepo, ndipo ankamuululira mau anga. Choncho iyeyo ankalemba makalata ondichititsa mantha aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuwonjezera apo, anthu ankasimba za ntchito zake zabwino ine ndili pomwepo ndipo anakamuwululira mawu anga. Choncho Tobiyayo ankatumiza makalata ondiopseza. |
Anamlembera chifukwa cha ichi, kuti ine ndichite mantha, ndi kuchita chotero, ndi kuchimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.
Pakuti ambiri mu Yuda analumbirirana naye chibwenzi; popeza ndiye mkamwini wake wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wake Yehohanani adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.
Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.
Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi;
Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.
Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.