Ndipo ndinazindikira kuti sanamtume Mulungu; koma ananena choneneracho pa ine, popeza Tobiya ndi Sanibalati adamlembera.
Nehemiya 6:11 - Buku Lopatulika Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? Ndani wonga ine adzalowa mu Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? Ndani wonga ine adzalowa m'Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ine ndidayankha kuti, “Munthu wonga ine nkuthaŵa kodi? Ndipo munthu wonga ine, kodi nkukabisala m'Nyumba ya Mulungu, kuti ndidzipulumutse? Zimenezo ai, toto, ine sindipitako!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ndinayankha kuti, “Kodi munthu ngati ine nʼkuthawa? Kapena munthu wofanana ndi ine nʼkupita ku Nyumba ya Mulungu kuti apulumutse moyo wake? Ayi, ine sindipita!” |
Ndipo ndinazindikira kuti sanamtume Mulungu; koma ananena choneneracho pa ine, popeza Tobiya ndi Sanibalati adamlembera.
Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindingathe kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani?
Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.
Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.
Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa ndipo zioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.
Ndipo adzanyeketsa ulemerero wa m'nkhalango yake, ndi wa m'munda wake wopatsa bwino, moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera.
Koma uike Aroni ndi ana ake aamuna, azisunga ntchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe.
Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.
Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.
Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali mu Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai.
Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;
pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.
Ndi chikhulupiriro anasiya Ejipito, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.
popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?