Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake.
Nehemiya 5:18 - Buku Lopatulika Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsire chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsira chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono chakudya cha pa tsiku limodzi chinali ichi: ng'ombe imodzi, nkhosa zisanu ndi imodzi zonenepa, ndiponso nkhuku zochuluka. Pa masiku khumi aliwonse panalinso matumba achikopa ochuluka a vinyo. Komabe ngakhale choncho, ine sindidafune kulandira chakudya chimene abwanamkubwa ankalandira, chifukwa chakuti anthu anga anali othinidwa kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lililonse pamaphikidwa ngʼombe imodzi, nkhosa zabwino zisanu ndi imodzi pamodzi ndi nkhuku. Ndipo pakutha pa masiku khumi aliwonse pankakhala matumba achikopa ochuluka a vinyo wa mitundu yonse. Ngakhale zinali choncho, Ine sindinatenge chakudya choperekedwa kwa bwanamkubwa, chifukwa izi zinali zosautsa anthu. |
Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake.
kapena sitinadye mkate chabe padzanja la munthu aliyense, komatu m'chivuto ndi chipsinjo, tinagwira ntchito usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu;