Chomwecho Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ake onse awiri.
Nehemiya 5:17 - Buku Lopatulika Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komanso masiku onse ndinkadyetsa anthu 150, Ayuda ndi akulu olamula, kuphatikizapo anthu amene adaabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ina yotizungulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuwonjezera apa, ndinkadyetsa Ayuda, akuluakulu kuphatikizanso anthu amene ankabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ya anthu otizungulira okwanira 150. |
Chomwecho Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ake onse awiri.
Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.
Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisraele onse kuphiri la Karimele, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a chifanizocho mazana anai, akudya pa gome la Yezebele.
Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake.
Ndiponso ndinalimbikira ntchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligule, ndi anyamata anga onse anasonkhanira ntchito komweko.