Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu,
Nehemiya 5:14 - Buku Lopatulika Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadye chakudya cha kazembe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadya chakudya cha kazembe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kuyambiranso nthaŵi imene adandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa m'dziko la Yuda, kuchokera chaka cha 20 mpaka chaka cha 32 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, ndiye kuti zaka khumi ndi ziŵiri, ineyo ndi abale anga sitidalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndiponso kuyambira nthawi imene anandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa wa dziko la Yuda, kuchokera chaka cha makumi awiri mpaka chaka cha 32 muulamuliro wa ufumu wa Aritasasita, ndiye kuti kwa zaka zokwana 12, ine ngakhale abale anga sitinalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa. |
Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu,
Koma pochitika ichi chonse sindinkakhale ku Yerusalemu; pakuti chaka cha makumi atatu ndi chachiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu ya Babiloni ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole;
Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse.
Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu.
Mphotho yanga nchiyani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.