Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Nehemiya 4:9 - Buku Lopatulika Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, chifukwa cha iwowa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, chifukwa cha iwowa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo ife tidapemphera kwa Mulungu wathu, ndipo tidaika alonda oti azititeteza kwa adani athuwo usana ndi usiku. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ife tinapemphera kwa Mulungu wathu ndipo tinayika alonda otiteteza kwa adaniwo usiku ndi usana. |
Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi lichuluka, motero sitidzakhoza kumanga lingali.
Nati adani athu, Sadzadziwa kapena kuona mpaka talowa pakati pao, ndi kuwapha, ndi kuleketsa ntchitoyi.
Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.
Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: