Momwemo tinalikugwira ntchito; gawo lina la iwo linagwira nthungo kuyambira mbandakucha mpaka zatuluka nyenyezi.
Nehemiya 4:22 - Buku Lopatulika Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Aliyense agone mu Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wake, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira ntchito usana. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Aliyense agone m'Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wake, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira ntchito usana. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa nthaŵi imeneyi ndidaŵauzanso anthu kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone m'Yerusalemu, kuti tikhale ndi otitchinjiriza usiku, ndipo kuti masana tizigwira ntchito.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi imeneyo ndinawuzanso anthuwo kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone mu Yerusalemu kuti tikhale ndi otilondera usiku ndi kuti masana tizigwira ntchito.” |
Momwemo tinalikugwira ntchito; gawo lina la iwo linagwira nthungo kuyambira mbandakucha mpaka zatuluka nyenyezi.
Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anavula zovala zake, yense anapita ndi chida chake kumadzi.