Ndipo anati, Akandiposa mphamvu Aaramu, udzandilanditsa ndiwe; koma akakuposa mphamvu ana a Amoni, ndidzakulanditsa ndine.
Nehemiya 4:20 - Buku Lopatulika paliponse mukumva mau a lipenga, musonkhanire komweko kwa ife; Mulungu wathu adzatigwirira nkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 paliponse mukumva mau a lipenga, musonkhanire komweko kwa ife; Mulungu wathu adzatigwirira nkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono kumene muliriko mukamva kulira kwa lipenga, mudzasonkhane msanga kumene tili ife kuno. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono kulikonse kumene muliko, mukamva kulira kwa lipenga bwerani mudzasonkhane kumene kuli ine kuno. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.” |
Ndipo anati, Akandiposa mphamvu Aaramu, udzandilanditsa ndiwe; koma akakuposa mphamvu ana a Amoni, ndidzakulanditsa ndine.
Ndipo ndinati kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Ntchito ndiyo yochuluka ndi yachitando, ndi ife tili palakepalake palingapo, yense atalikizana ndi mnzake;
Momwemo tinalikugwira ntchito; gawo lina la iwo linagwira nthungo kuyambira mbandakucha mpaka zatuluka nyenyezi.
Ndipo anagulula njinga za magaleta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aejipito anati, Tithawe pamaso pa Israele; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aejipito.
Pamenepo Yehova adzatuluka, nadzachita nkhondo ndi amitundu aja, monga anachitira nkhondo tsiku lakudumana.
Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, Iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu;
pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani.
Munthu mmodzi wa inu adzapirikitsa anthu chikwi chimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.