ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.
Nehemiya 3:32 - Buku Lopatulika Ndi pakati pa chipinda chosanja cha kungodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza osula golide ndi ochita malonda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi pakati pa chipinda chosanja cha kungodya ndi chipata chankhosa anakonza osula golide ndi ochita malonda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo pakati pa chipinda chapamwamba chapangodya ndi Chipata cha Nkhosa, amisiri a golide ndi anthu amalonda adakonza chigawo chao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo pakati pa chipinda chapamwamba chapangodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza ndi amisiri a golide ndi anthu amalonda. |
ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata cha Nsomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka ku Chipata cha Nkhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi.
Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.
Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golide kufikira kunyumba ya antchito a m'kachisi, ndi ya ochita malonda, pandunji pa Chipata cha Hamifikadi, ndi kuchipinda chosanja cha kungodya.
Pambali pake anakonza Uziyele mwana wa Haraya, wa iwo osula golide. Ndi padzanja pake anakonza Hananiya, wa iwo osanganiza zonunkhira; nalimbikitsa Yerusalemu mpaka linga lachitando.
Koma pali thamanda mu Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa mu Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu.