Ndinaikanso osunga chuma, asunge nyumba za chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao.
Nehemiya 3:30 - Buku Lopatulika Potsatizana naye Hananiya mwana wa Selemiya, ndi Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, anakonza gawo lina. Potsatizana naye anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya pandunji pa chipinda chake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potsatizana naye Hananiya mwana wa Selemiya, ndi Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, anakonza gawo lina. Potsatizana naye anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya pandunji pa chipinda chake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambali pa iyeyo Hananiya, mwana wa Selemiya, ndiponso Hanuni, mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Mesulamu, mwana wa Berekiya, adakonza chigawo choyang'anana ndi chipinda chake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Hananiya mwana wa Selemiya ndiponso Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi anakonza chigawo china. Motsatana naye, Mesulamu mwana wa Berekiya anakonza chigawo choyangʼanana ndi chipinda chake. |
Ndinaikanso osunga chuma, asunge nyumba za chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao.
Potsatizana nao anakonza Zadoki mwana wa Imeri pandunji pa nyumba yake. Ndi potsatizana naye anakonza Semaya mwana wa Sekaniya, wosunga Chipata cha Kum'mawa.
Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golide kufikira kunyumba ya antchito a m'kachisi, ndi ya ochita malonda, pandunji pa Chipata cha Hamifikadi, ndi kuchipinda chosanja cha kungodya.
Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana.
Pakuti ambiri mu Yuda analumbirirana naye chibwenzi; popeza ndiye mkamwini wake wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wake Yehohanani adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.