Pamenepo anaimirira pamodzi Yesuwa ndi ana ake ndi abale ake, Kadimiyele ndi ana ake, ana a Yuda, kuyang'anira ogwira ntchito m'nyumba ya Mulungu, ana a Henadadi ndi ana ao ndi abale ao Alevi.
Nehemiya 3:24 - Buku Lopatulika Potsatizana naye Binuyi mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira kunyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungodya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potsatizana naye Binuyi mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira kunyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungodya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambali pa iyeyo Binuyi, mwana wa Henadadi, adakonza chigawo china, kuyambira ku nyumba ya Azariya mpaka kukafika ku Ndonyo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Motsatana naye, Binuyi mwana wa Henadadi anakonzanso chigawo china, kuchokera pa nyumba ya Azariya kukafika potsirizira pa ngodya. |
Pamenepo anaimirira pamodzi Yesuwa ndi ana ake ndi abale ake, Kadimiyele ndi ana ake, ana a Yuda, kuyang'anira ogwira ntchito m'nyumba ya Mulungu, ana a Henadadi ndi ana ao ndi abale ao Alevi.
Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubu mwana wa Pahatimowabu, anakonza gawo lina, ndi Nsanja ya Ng'anjo.
Ndi pa mbali pake Ezere mwana wa Yesuwa, mkulu wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera kunyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga.
Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubu pandunji pa nyumba pao. Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maaseiya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yake.
Potsatizana nao Atekowa anakonza gawo lina, pandunji pa nsanja yaikulu yosomphoka ndi kulinga la Ofele.