Nehemiya 3:21 - Buku Lopatulika Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uriya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira kukhomo la nyumba ya Eliyasibu kufikira malekezero ake a nyumba ya Eliyasibu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uriya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira kukhomo la nyumba ya Eliyasibu kufikira malekezero ake a nyumba ya Eliyasibu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambali pa iyeyo Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi, adakonza chigawo china kuyambira ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mpaka ku mathero a nyumbayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Motsatana naye, Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi anakonzanso chigawo china kuchokera ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mpaka kumapeto kwake. |
Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa dzina lao.
Ndipo pa tsiku lachinai siliva ndi golide ndi zipangizo zinayesedwa m'nyumba ya Mulungu wathu, m'dzanja la Meremoti mwana wa Uriya wansembe, ndi pamodzi naye Eleazara mwana wa Finehasi, ndi pamodzi nao Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadiya mwana wa Binuyi, Alevi;
Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.
Potsatizana naye Baruki mwana wa Zabai anafulumira kukonza gawo lina kuyambira popindirira mpaka kukhomo la nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe.
Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana.
Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa ndi dzina lao.