Nehemiya 3:20 - Buku Lopatulika Potsatizana naye Baruki mwana wa Zabai anafulumira kukonza gawo lina kuyambira popindirira mpaka kukhomo la nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potsatizana naye Baruki mwana wa Zabai anafulumira kukonza gawo lina kuyambira popindirira mpaka kukhomo la nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambali pa iyeyo Baruki mwana wa Zabai adakonza chigawo kuyambira pa Ndonyo mpaka ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu, mkulu wa ansembe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Motsatana naye, Baruki mwana wa Zakai anakonzanso chigawo china kuchokera pa ngodya mpaka pa chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe. |
Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine.
Chinkana ichi, Eliyasibu wansembe, woikidwa asunge zipinda za nyumba ya Mulungu wathu, anachita chibale ndi Tobiya,
Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.
Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uriya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira kukhomo la nyumba ya Eliyasibu kufikira malekezero ake a nyumba ya Eliyasibu.
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.