Nehemiya 3:11 - Buku Lopatulika Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubu mwana wa Pahatimowabu, anakonza gawo lina, ndi Nsanja ya Ng'anjo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubu mwana wa Pahatimowabu, anakonza gawo lina, ndi Nsanja ya Ng'anjo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Malikiya, mwana wa Harimu, ndiponso Hasubu mwana wa Pahatimowabu, adakonza chigawo china pamodzi ndi Nsanja ya Ng'anjo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Malikiya mwana wa Harimu ndi Hasubu mwana wa Pahati-Mowabu anakonzanso chigawo china ndiponso Nsanja ya Ngʼanjo. |
Ana a Pahatimowabu, a ana a Yesuwa ndi Yowabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi awiri.
Wa ana a Pahatimowabu, Eliehoenai mwana wa Zerahiya; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri.
Ndi gulu lina la oyamikira linamuka mokomana nao, ndi ine ndinawatsata, pamodzi ndi limodzi la magawo awiri la anthu palinga, napitirira pa Nsanja ya Ng'anjo, mpaka kulinga lachitando;
Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafa, pandunji pa nyumba yake. Ndi pambali pake anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya.
Ana a Pahatimowabu, a ana a Yesuwa ndi Yowabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi limodzi ndi asanu ndi atatu.