Nehemiya 3:10 - Buku Lopatulika Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafa, pandunji pa nyumba yake. Ndi pambali pake anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafa, pandunji pa nyumba yake. Ndi pambali pake anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambali pa iwowo Yedaya, mwana wa Harumafa, adakonza chigawo choyang'anana ndi nyumba yake. Pambali pa iyeyo Hatusi, mwana wa Hasabuneiya, adakonza chigawo china. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kulumikiza ichi, Yedaya mwana wa Harumafi anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba yake, ndipo Hatusi mwana wa Hasabaneya anakonzanso motsatana naye. |
Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubu mwana wa Pahatimowabu, anakonza gawo lina, ndi Nsanja ya Ng'anjo.
Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubu pandunji pa nyumba pao. Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maaseiya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yake.
Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu.
Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.