Chifukwa chake tsono manja anu alimbike, nimuchite chamuna; pakuti Saulo mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao.
Nehemiya 2:18 - Buku Lopatulika Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero ndidaŵasimbira za m'mene Mulungu wanga adandithandizira ndiponso mau amene mfumu idandiwuza. Apo anthuwo adati, “Tiyeni tiyambepo kumanga.” Choncho adalimbitsana mtima kuti akaiyambe ntchito yabwinoyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinawawuza za mmene Yehova Mulungu wanga anandichitira zabwino ndiponso mawu amene mfumu inandiwuza. Tsono anati, “Tiyeni tiyambenso kumanga.” Kotero analimbitsana mtima kuti ayambenso ntchito yabwinoyi. |
Chifukwa chake tsono manja anu alimbike, nimuchite chamuna; pakuti Saulo mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao.
Akulu a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye mu ufumu wake, pamodzi ndi Aisraele onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israele, ndi awa.
Limbika mtima, tilimbikire anthu athu, ndi mizinda ya Mulungu wathu; ndipo Yehova achite chomkomera.
Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m'mzinda wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka.
nasunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asiriya, kulimbitsa manja ao mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israele.
ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya kuzipata za linga lili ku Kachisi, ndi ya linga la mzinda, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira.
pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.
Ndipo Yonatani mwana wa Saulo ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu.