Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kuchipululu.
Nehemiya 2:15 - Buku Lopatulika Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang'ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa Chipata cha ku Chigwa, momwemo ndinabwereranso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang'ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa Chipata cha ku Chigwa, momwemo ndinabwereranso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho ndidayenda ndi usiku kudzera ku chigwa, kunka ndikuliyang'ana khomalo. Ndipo ndidapotoloka nkudzaloŵa mu mzinda kudzera pa Chipata cha ku Chigwa chija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero usikuwo ndinapita ku chigwa, ndikuyangʼana khomalo. Pomaliza ndinabwerera ndi kukalowanso mu mzinda kudzera ku Chipata cha ku Chigwa. |
Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kuchipululu.
Uziya anamanganso nsanja mu Yerusalemu pa Chipata cha Kungodya, ndi pa Chipata cha ku Chigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa.
Koma olamulira sanadziwe uko ndinamuka, kapena chochita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufulu, kapena olamulira, kapena otsala akuchita ntchitoyi.
Chipata cha ku Chigwa anachikonza Hanuni; ndi okhala mu Zanowa anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso mikono chikwi chimodzi cha lingalo mpaka ku Chipata cha Kudzala.
M'mene Yesu adanena izi, anatuluka ndi ophunzira ake, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kidroni, kumene kunali munda, umene analowamo Iye ndi ophunzira ake.