Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu.
Nehemiya 13:8 - Buku Lopatulika Ndipo ndinaipidwa nacho kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwachotsa m'chipindamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinaipidwa nacho kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwachotsa m'chipindamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo ndidapsa mtima kwambiri, ndipo ndidamtaya kunja katundu yense wa Tobiya amene anali m'chipindamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinapsa mtima kwambiri ndipo ndinataya kunja katundu yense wa Tobiya amene anali mʼchipindamo. |
Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu.
Pamenepo ndinalamulira, ndipo anayeretsa zipindazo; ndipo ndinabwezeramonso zipangizo za nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zopereka za ufa ndi lubani.
Pakuti changu cha pa nyumba yanu chandidya; ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.