Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiye Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m'ntchito mwao,
Nehemiya 13:30 - Buku Lopatulika Momwemo ndinawayeretsa kuwachotsera achilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense kuntchito yake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemo ndinawayeretsa kuwachotsera achilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense kuntchito yake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Umu ndimo m'mene ndidaŵayeretsera anthu poŵachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndidakhazikitsa ntchito za ansembe ndi za Alevi, kuti aliyense adziŵe bwino ntchito yake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Motero ndinayeretsa ansembe ndi Alevi powachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndinakhazikitsa ntchito zawo, kuti aliyense akhale pa ntchito yake. |
Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiye Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m'ntchito mwao,
ndi kuti sitidzapereka ana athu aakazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu aamuna ana ao aakazi;