Ndipo aliyense wosachita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpirikitsa m'dziko, kapena kumlanda chuma chake, kapena kummanga m'kaidi.
Nehemiya 13:21 - Buku Lopatulika Koma ndinawachitira umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? Mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikenso pa Sabata. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndinawachitira umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? Mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikenso pa Sabata. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ndidaŵachenjeza ndipo ndidaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Mukachitanso zimenezi ndidzakumangani.” Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka m'tsogolo mwake, anthuwo sadabwerenso pa tsiku la sabata. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ndinawachenjeza ndi kuwafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Ngati muchitanso zimenezi, ine ndidzakugwirani.” Kuyambira nthawi imeneyo, sanabwerenso pa tsiku la Sabata. |
Ndipo aliyense wosachita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpirikitsa m'dziko, kapena kumlanda chuma chake, kapena kummanga m'kaidi.
Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu;
Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'choponderamo tsiku la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo mu Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya.
Momwemo eni malonda ndi ogulitsa malonda ali onse, anagona kunja kwa Yerusalemu kamodzi kapena kawiri.
kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino.