Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu;
Nehemiya 13:18 - Buku Lopatulika Sanatero kodi makolo anu, ndipo Mulungu wathu anatifikitsira ife ndi mzinda uno choipa ichi chonse? Koma inu muonjezera Israele mkwiyo pakuipsa Sabata. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sanatero kodi makolo anu, ndipo Mulungu wathu anatifikitsira ife ndi mudzi uno choipa ichi chonse? Koma inu muonjezera Israele mkwiyo pakuipsa Sabata. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Makolo anu adachitanso motero momwemu, ndipo Mulungu wathu adadzetsa chiwonongeko pa ife ndi pa mzinda uno. Koma inu mukufuna kuutsanso mkwiyo wa Chauta pa Aisraele, pamene mukuipitsa tsiku la sabata motere.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Makolo anu anachita zomwezi ndipo Mulungu wathu anadzetsa mavuto pa ife ndi pa mzinda uwu. Kodi inu mukufuna kuwutsanso mkwiyo wa Mulungu pa Israeli pamene mukudetsa tsiku la Sabata?” |
Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu;
Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zakezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.
Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.
Chifukwa mwafukiza, ndi chifukwa mwachimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'chilamulo chake, ndi m'malemba ake, ndi m'mboni zake, chifukwa chake choipachi chakugwerani, monga lero lomwe.
Kodi mwaiwala zoipa za makolo anu, ndi zoipa za mafumu a Yuda, ndi zoipa za akazi ao, ndi zoipa zanu, ndi za akazi anu, zimene anazichita m'dziko la Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu?
Sanalekenso zigololo zake zochokera ku Ejipito, pakuti anagona naye mu unamwali wake, nakhudza mawere a unamwali wake, namtsanulira chigololo chao.
Ndipo mukapanda kundimvera, zingakhale izi, ndidzaonjeza kukulangani kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.
Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.
Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga;
Ndipo taonani, mwauka m'malo mwa makolo anu, gulu la anthu ochimwa, kuonjezanso mkwiyo waukali wa Yehova pa Israele.