Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m'manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika.
Nehemiya 13:13 - Buku Lopatulika Ndinaikanso osunga chuma, asunge nyumba za chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinaikanso osunga chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo ndidasankha aŵa kuti akhale asungachuma: wansembe Selemiya, mlembi Zadoki ndiponso Pedaya mmodzi mwa Alevi, kudzanso mthandizi wao Hanani, mwana wa Zakuri, mdzukulu wa Mataniya, popeza kuti ndidaadziŵa kuti anthuwo anali okhulupirika. Ntchito yao inali yogaŵira abale ao zinthu zofunika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ndinasankha wansembe Selemiya, mlembi Zadoki, ndi Mlevi wotchedwa Pedaya kukhala oyangʼanira zipinda zosungiramo. Ndinasankhanso Hanani mwana wa Zakuri mwana wa Mataniya kukhala wowathandizira chifukwa ndinaona kuti anthu awa anali odalirika. Ntchito yawo inali yogawira abale awo zinthu zofunika. |
Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m'manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika.
Ndalama za nsembe zopalamula ndi ndalama za nsembe yauchimo sanabwere nazo kunyumba ya Yehova; nza ansembe izi.
Koma sanawawerengere ndalamazo zoperekedwa m'dzanja lao, pakuti anachita mokhulupirika.
Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzilimodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzilimodzi la magawo khumi kunyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, kunyumba ya chuma.
Ndipo woyang'anira wa Alevi mu Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oimbira ena anayang'anira ntchito ya m'nyumba ya Mulungu.
ndi ana ena a ansembe ndi malipenga: Zekariya mwana wa Yonatani, mwana wa Semaya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu,
Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za chuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzilimodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi chilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi akuimirirako.
Potsatizana naye Hananiya mwana wa Selemiya, ndi Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, anakonza gawo lina. Potsatizana naye anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya pandunji pa chipinda chake.
ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.
Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.
Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitao wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yake?
Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.
Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.
Ndimyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,