Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawatulukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba mbiri.
Nehemiya 12:7 - Buku Lopatulika Salu, Amoki, Hilikiya, Yedaya. Awa ndi akulu a ansembe ndi abale ao m'masiku a Yesuwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Salu, Amoki, Hilikiya, Yedaya. Awa ndi akulu a ansembe ndi abale ao m'masiku a Yesuwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Salu, Amoki, Hilikiya, ndi Yedaya. Ameneŵa anali atsogoleri pakati pa ansembe ndi achibale ao pa nthaŵi ya Yesuwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Salu, Amoki, Hilikiya ndi Yedaya. Awa ndiye anali atsogoleri a ansembe ndi abale awo pa nthawi ya Yesuwa. |
Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawatulukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba mbiri.
Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israele, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu.
Ndipo ansembe ndi Alevi amene anakwera ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa, ndi awa: Seraya, Yeremiya, Ezara,
Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko.
Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,
Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima padzanja lake lamanja, atsutsana naye.