Inu ndinu akulu a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele ku malo ndalikonzera.
Nehemiya 12:12 - Buku Lopatulika Ndi m'masiku a Yoyakimu ansembe aakulu a nyumba za makolo ndiwo: wa Seraya, Meraya; wa Yeremiya, Hananiya; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi m'masiku a Yoyakimu ansembe aakulu a nyumba za makolo ndiwo: wa Seraya, Meraya; wa Yeremiya, Hananiya; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa nthaŵi ya Yoyakimu, mkulu wa ansembe, atsogoleri a mabanja a ansembe anali aŵa: Mtsogoleri wa fuko la Seraya anali Meraya. Wa fuko la Yeremiya, anali Hananiya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi ya Yowakimu, awa ndiwo anali atsogoleri a mabanja a ansembe: Mtsogoleri wa fuko la Seraya anali Meraya; wa fuko la Yeremiya anali Hananiya; |
Inu ndinu akulu a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele ku malo ndalikonzera.
Ndipo anapeza kuti amuna aakulu a ana a Eleazara anachuluka, a ana a Itamara anachepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akulu a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu.
M'masiku a Eliyasibu, Yoyada, Yohanani, ndi Yaduwa, Alevi analembedwa akulu a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariusi wa ku Persiya.