Ana a Benjamini omwe, kuyambira ku Geba pa Mikimasi, ndi Aya, ndi pa Betele ndi midzi yake,
Nehemiya 11:32 - Buku Lopatulika pa Anatoti, Nobi, Ananiya, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pa Anatoti, Nobi, Ananiya, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anatoti, Nobi, Ananiya, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ku Anatoti, Nobu ndi Ananiya, |
Ana a Benjamini omwe, kuyambira ku Geba pa Mikimasi, ndi Aya, ndi pa Betele ndi midzi yake,
Lero lomwe adzaima pa Nobu; agwedezera dzanja lake paphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu.
Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;
Ndipo Davide anafika ku Nobu kwa Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?
Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira ntchito, ninena nane, Asadziwe munthu aliyense kanthu za ntchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.
Ndipo anakantha Nobu ndiwo mzinda wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu aamuna ndi aakazi, ana ndi makanda, ng'ombe ndi abulu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa.