Ndi kunena za chakudya chake, panali chakudya chosalekeza chopatsidwa kwa iye ndi mfumu, tsiku lililonse gawo lake, masiku onse a moyo wake.
Nehemiya 11:23 - Buku Lopatulika Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oimbira chowathandiza, yense chake pa tsiku lake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oimbira chowathandiza, yense chake pa tsiku lake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti mfumu idaalamula kuti magulu oimbawo azikhalapo tsiku ndi tsiku, potsogolera maimbidwe a nyimbo za m'Nyumba ya Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti mfumu inalamula kuti tsiku ndi tsiku pa nthawi zachipembedzo oyimba nyimbowo azikhalapo. |
Ndi kunena za chakudya chake, panali chakudya chosalekeza chopatsidwa kwa iye ndi mfumu, tsiku lililonse gawo lake, masiku onse a moyo wake.
Ndipo awa ndi oimba, akulu a nyumba za makolo a Alevi, okhala m'zipinda, omasuka ku ntchito zina; pakuti anali nayo ntchito yao usana ndi usiku.
Ndi Aisraele onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.