Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwaomwao m'mizinda mwao, ndiwo Israele, ansembe, Alevi, ndi Antchito a m'kachisi.
Nehemiya 11:21 - Buku Lopatulika Koma antchito a m'kachisi anakhala mu Ofele, ndi Ziha, ndi Gisipa anali oyang'anira antchito a m'kachisi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Anetini anakhala m'Ofele, ndi Ziha, ndi Gisipa anali oyang'anira Anetini. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu ankakhala ku Ofele, mu Yerusalemu, ndipo Ziha ndi Gisipa ankaŵayang'anira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma antchito a ku Nyumba ya Mulungu ankakhala pa phiri la Ofeli, ndipo Ziha ndi Gisipa ndiwo anali kuwayangʼanira. |
Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwaomwao m'mizinda mwao, ndiwo Israele, ansembe, Alevi, ndi Antchito a m'kachisi.
Anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofele anamanga kwakukulu.
Koma antchito a m'kachisi okhala mu Ofele anakonza kufikira kumalo a pandunji pa Chipata cha Madzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo.
Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golide kufikira kunyumba ya antchito a m'kachisi, ndi ya ochita malonda, pandunji pa Chipata cha Hamifikadi, ndi kuchipinda chosanja cha kungodya.