Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Nehemiya 11:2 - Buku Lopatulika

Ndipo anthu anadalitsa amuna onse akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala mu Yerusalemu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anthu anadalitsa amuna onse akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala m'Yerusalemu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo anthu adayamika anzao onse amene adadzipereka kuti azikhala ku Yerusalemu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Anthu anayamikira onse amene anadzipereka kuti azikhala mu Yerusalemu.

Onani mutuwo



Nehemiya 11:2
8 Mawu Ofanana  

Mzindawo tsono ndi wachitando, ndi waukulu; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.


Dalitso la iye akati atayike linandidzera, ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauimbitsa mokondwera.


ngati ziuno zake sizinandiyamike, ngati sanafunde ubweya wa nkhosa zanga;


Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.


Mupempherere mtendere wa Yerusalemu; akukonda inu adzaona phindu.


polowa dzuwa mumbwezeretu chikolecho, kuti agone m'chovala chake, ndi kukudalitsani; ndipo kudzakukhalirani chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu.


Mtima wanga uvomerezana nao olamulira a mu Israele, amene anadzipereka mwaufulu mwa anthu. Lemekezani Yehova.